Klemen Pisk

poet, writer, translator and musician

Poem in Chewa

Myendayekha ndi Nkhandwe

Tsiku lina Myendayekha adalemba mzere mun’chenga,
ndipo adati kwa Nkhandwe:
“Usayelekeze kulumpha mzerewu.”
Kenaka adajambula bwalo mozungulira Nkhandweyo,
naiuzanso kuti: ”Osatuluka m’bwalomu.
Ukhoza kuyendayenda koma usadumphe
mzere wa malire abwaloli.”
Posachedwa mphepo ya mkuntho
idaomba ndipo mizere ija idafufutika.
Nkhandwe idali chikhalire m’bwalo muja.
Chisanu ndi mvula zidaikhaulitsa, koma sidasunthe.
Siidadziwe ngati malire aja adalipobe,
pomwe utafufutika ndi mphepo mumchenga muja.

Translated into Chewa by Ezekiel Peter Ching'oma